Ndandanda ya Mlungu wa January 14
MLUNGU WA JANUARY 14
Nyimbo 52 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 17 ndime 15-19 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Mateyu 7-11 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 10:24-42 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Muzicita Zinthu Mwanzelu Ndipo Muzipewa Zinthu Zopanda Pake—1 Sam. 12:21; Miy. 23:4, 5 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi ndi Zinthu Ziti Zimene Tiyenela Kuchula Tikamapemphela?—rs tsa. 341 ndime 8–tsa. 342 ndime 6 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 73
Mph. 10: Athandizeni pa Zosoŵa Zao. Nkhani yocokela m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 188, ndime 4, mpaka tsamba 189, ndime 4. Mwacidule funsani wofalitsa amene wapita patsogolo cifukwa cakuti ena anamuonetsa cidwi.
Mph. 10: Kodi Tiphunzilapo Ciani? Kukambilana. Lemba la Mateyu 4:1-11 liŵelengedwe. Kambilanani mmene nkhani ili pa lembali ingatithandizile mu ulaliki.
Mph. 10: “Citilani Umboni Mokwanila.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 92 ndi Pemphelo