“Citilani Umboni Mokwanila”
1. Kodi n’citsanzo cabwino cotani cimene mtumwi Paulo anapeleka muulaliki?
1 ‘Kwanilitsani mbali zonse za utumiki wanu.’ (2 Tim. 4:5) Polankhula mau olimbikitsa amenewa, mosakaikila mtumwi Paulo anali ndi ufulu wolankhula kwa Timoteyo. Paulo anamaliza maulendo ake atatu a umishonale, pakati pa zaka za 47 ndi 56 C.E. Buku la Macitidwe limachula mobweleza-bweleza kuti Paulo anacitila “umboni mokwanila.” (Mac. 23:11; 28:23) Nanga masiku ano tingacite bwanji zimenezi?
2. Kodi tingapeleka bwanji umboni mokwanila polalikila kunyumba ndi nyumba?
2 Kunyumba ndi Nyumba: Kuti tifikile eninyumba amene sanamvepo uthenga wabwino, tingafunike kusintha nthawi yowafikila. Amuna angapezeke panyumba m’madzulo kapena kumapeto a mlungu. Tiyenela kuyesetsa kukamba ndi munthu pa khomo lililonse, ndi kubwelelako kumakhomo kumene anthu sapezeka-pezeka. Koma bwanji ngati zoyesa-yesa zanu siziphula kanthu? Mwina kulemba kalata kapena kutuma foni kungathandize.
3. Kodi inu muli ndi mipata yotani yocitila umboni poyela ndi mwamwai?
3 Poyela ndi Mwamwai: Masiku ano, atumiki a Yehova akulengeza “nzelu yeni-yeni” kwa onse amene afuna kumvela. Nthawi zina amacita zimenezi “mumseu” kapena “m’mabwalo a mzinda.” (Miy. 1:20, 21)[1] Kodi timakhala chelu kuti ticitile umboni pogwila nchito zathu za tsiku ndi tsiku? Kodi ndife ‘otangwanika kwambili ndi nchito yolalikila mau a Mulungu’? (Mac. 18:5) Ngati nditelo, ndiye kuti tikukwanilitsa udindo wathu ‘wocitila umboni mokwanila.’—Mac. 10:42; 17:17; 20:20, 21, 24.
4. Kodi pemphelo ndi kusinkha-sinkha, zingatithandize bwanji kucitila umboni mokwanila?
4 Koma, nthawi zina cifukwa ca zofooko zathu kapena mwina cifukwa ca manyazi acibadwa, tingazengeleze kucitila umboni. Koma zoona n’zakuti, Yehova amadziŵa zolephela zathu. (Sal. 103:14) Conco, ngati zinthu zotelo zaticitikila, tingapemphele kwa iye kuti tilalikile molimba mtima. (Mac. 4:29, 31) Ndiponso, pocita phunzilo laumwini ndi pamene tisinkha-sinkha Mau a Mulungu, colinga cathu cizikhala kukulitsa ciyamikilo cathu ca uthenga wabwino umene ndi cinthu ca mtengo wapatali. (Afil. 3:8) Izi zidzatithandiza kuti tizilalikila mwacangu.
5. Kodi tingacite ciani pokwanilitsa ulosi wa Yoweli?
5 Ulosi wa Yoweli unanenelatu kuti, tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova lisanabwele, anthu a Mulungu adzapitilizabe kulalikila ndipo sadzabwelela m’mbuyo. (Yow. 2:2, 7-9) Conco, tiyeni tonse ticite zimene tingathe pa nchito yolalikila iyi imene sidzakacitikanso.