Ndandanda ya Mlungu wa January 21
MLUNGU WA JANUARY 21
Nyimbo 61 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 18 ndime 1-5, ndi mabokosi patsamba 142 ndi 144 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Mateyu 12-15 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 14:23–15:11 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Ngati Wina Wanena Kuti, ‘Ngati Mukufuna Kundilalikila Uthenga Wanu, Mupemphele Kaye’—rs tsa. 342 ndime 7-8 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tikuphunzilapo Ciani pa Citsanzo ca Isaki Cokonda Kucita Zinthu Mwamtendele?—Gen. 26:19-22 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 32
Mph. 10: Lengezani Uthenga Wabwino Mwakhama. (Mac. 5:42) Kambilanani ndi wofalitsa mmodzi kapena aŵili acangu. Afunseni kuti afotokoze zimene zawathandiza kuona ulaliki kukhala wofunika. Kodi amacita ciani kuti akonzekele ulaliki? Nanga ulaliki wawathandiza bwanji kukhala olimba kuuzimu?
Mph. 10: Khalidwe Lathu Labwino Limapeleka Umboni. (1 Pet. 2:12) Kukambilana kozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012 tsa. 6-8, ndi Nsanja ya Olonda ya February 15, 2011 tsa. 29-30, ndime 13-16. Pemphani omvela kuti asimbe zimene aphunzilapo.
Mph. 10: “Kavalidwe Koyenela Kamalemekeza Mulungu.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 96 ndi Pemphelo