LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 1/13 tsa. 2
  • Kavalidwe Koyenela Kamalemekeza Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kavalidwe Koyenela Kamalemekeza Mulungu
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 1/13 tsa. 2

Kavalidwe Koyenela Kamalemekeza Mulungu

1. N’cifukwa ciani tiyenela kusamala mmene timaonekela?

1 Popeza ndife Akristu, masiku onse a anthu amaona zocita zathu. (1 Akor. 4:9) Tingaonetse kuti timaopa Mulungu ndi kuyamikila zinthu za kuuzimu zimene Yehova amatigaŵila, mwa kavalidwe kathu ndi mmene timazikongoletsela.—Sal. 116:12, 17.

2. Kodi Akristu amayaona motani masitaelo amene afala m’dzikoli?

2 Zovala Zaudongo ndi Zolongosoka: Maonekedwe athu ayenela kuonetsa kuti timatsatila mfundo za Mulungu wathu, amene ndi woyela ndi wadongosolo. (1 Akor. 14:33; 2 Akor. 7:1) Matupi athu, tsitsi lathu ndi zikhadabu zathu, ziyenela kukhala za ukhondo, ndipo tiyenela kuoneka bwino. Masiku ano mavalidwe osayenela afala. Sitiyenela kutengela mavalidwe oipa, cabe cifukwa cakuti woimba nyimbo kapena katswili wa zamaseŵela ndi mmene amavalila. Ngati timatsatila ciliconse cabwela m’fashoni, anthu angalephele kusiyanitsa pakati pa munthu amene amatumikila Mulungu ndi amene sam’tumikila.—Mal. 3:18.

3. Kodi ndi malemba ati amene amatiunikila za mmene tiyenela kuvalila?

3 Kavalidwe Koyenelela Atumiki Acikritsu: Pamene mtumwi Paulo analembela oyang’anila Wacikristu Timoteyo, iye analimbikitsa kuti “akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenela, povala mwaulemu ndi mwanzelu. . . Koma azidzikongoletsa mogwilizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenela kudzikongoletsela. Azidzikongoletsa ndi nchito zabwino.” (1 Tim. 2:9, 10) Uphungu umenewu umagwilanso nchito kwa amuna. Kuti titsimikize kuti mavalidwe athu ndi oyenela, tifunika kuganizilapo tisanavale. Zovala ziyenela kukhala zaudongo, zaukhondo ndi zaulemu, osati zodzionetsela, zodzutsa cilako-lako ca kugonana, kapena zokhumudwitsa ena.—1 Pet. 3:3.

4, 5. Posankha zovala, kodi tiyenela kukumbukila ciani?

4 Kuvala kwa ulemu kumayamba ndi kugula mwanzelu. Kudziŵa saizi ya zovala zathu ndi kupewa kusankha zovala zothina n’kofunika. Zovala zathu zili ngati masipika. Kuvala zothina kungayelekezeledwe ndi kukweza kwambili voliyamu. Kodi kucita zimenezo sikungakhumudwitse ena? Kodi zimenezo sizingaonetse kuti timatsogoleledwa ndi mzimu wa dziko wosadzilemekeza?

5 Ambili a ife timavala zovala za kaunjika. Koma popeza kuti zovala za pa kaunjika ndi zosavuta kupeza ndipo ndi zochipa, si zifukwa zokha zozigulila. Kusankha zovala za saizi yathu, zosalemba-lemba ndi zosaonetsa mzimu wa dziko, kumafuna nthawi. Komabe, abale athu ndiponso Yehova amayamikila zoyesa-yesa zathu pamene tisankha zovala zoyenelela.—1 Akor.10:31.

6. Kodi kavalidwe kathu kabwino ndi kudzikonza kwathu kuli ndi ubwino wanji?

6 Monga mmene kumwetulila kumakongoletsela nkhope, kavalidwe kathu ndi maonekedwe athu abwino nazonso, zimalemekeza uthenga umene timalalikila ndi gulu limene timaimila. Ena amene amationa pamene tili muulaliki, tipita kumisonkhano, ndi pamene tili panyumba, angafune kudziŵa cifukwa cake ndife osiyana ndi ena. Conco, anganene kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva [ndipo taona] kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zek. 8:23) Tiyeni tonse tionetse kuti timaopa Yehova mwa kavalidwe kanthu ndi mmene timadzikonzela.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani