Ndandanda ya Mlungu wa March 11
MLUNGU WA MARCH 11
Nyimbo 68 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 20 ndime 1-7, onani bokosi pa tsa. 156 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Maliko 13–16 (Mph. 10)
Na. 1: Maliko 14:22-42 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: N’cifukwa Ciani Tiyenela Kukumbukila Imfa ya Yesu?—rs tsa. 70 ndime 3-tsa. 71 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Zizindikilo za pa Cikumbutso Zimaimila Ciani?—rs tsa. 71 ndime 2-tsa. 72 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 109
Mph. 10: Tiphunzilapo Ciani? Ŵelengani Mateyu 10:7-10 ndi Luka 10:1-4, ndipo kambilanani mmene malembawa angatithandizile mu utumiki.
Mph. 10: Njila Zoonjezela Utumiki Wanu—Gawo 1. Nkhani yokambilana yocokela m’buku la Gulu, patsamba 111, ndime 1, mpaka tsamba 112, ndime 2. Funsani wofalitsa mmodzi kapena aŵili amene asamukila ku dela lina kapena amene aphunzila cinenelo cina n’colinga coonjezela utumiki wao. Kodi anakumana ndi mavuto otani? Ndipo anacita bwanji kuti awathetse? Kodi banja lao kapena mpingo unawathandiza bwanji? Kodi apeza madalitso otani?
Mph. 10: “Konzekelani Cikumbutso ndi Mtima Wacimwemwe.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Chulani makonzedwe a Cikumbutso amene mpingo wapanga. Pelekani lipoti loonetsa mmene nchito yoitanila anthu ku Cikumbutso ikuyendela pampingo panu.
Nyimbo 8 ndi Pemphelo