Konzekelani Cikumbutso ndi Mtima Wacimwemwe
1. Kodi nyengo ya Cikumbutso ndi nthaŵi yapadela yocita ciani?
1 Cikumbutso cimene cidzacitika pa Ciŵili, March 26, cidzatipatsa mwai wofunika kwambili wokhalila acimwemwe pa zimene Mulungu anaticitila kuti atipulumutse. (Yes. 61:10) Mtima wacimwemwe udzatithandiza kukhala okonzekela bwino kwambili ngakhale Cikumbutso cisanacitike. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?
2. N’ciani cimatilimbikitsa kuti tikonzekele za Cikumbutso?
2 Kukonzekela Cikumbutso: Mgonelo wa Ambuye ndi mwambo waukulu kwambili koma wosavuta kucita. Ngakhale n’conco, pamafunika kukonzekela pasadakhale kuti tisanyalanyaze mfundo zonse zofunika kwambili. (Miy. 21:5) Muyenela kusankha nthawi ndi malo oyenelela pamene padzacitikila mwambo umenewu. Muyenela kukhala ndi ziphiphilitso zoyenela. Malo amene padzacitikila Cikumbutso ayenela kuyeletsedwa ndi kukonzedwa bwino-bwino. Mkambi ayenela kukonzekela bwino, ndipo abale opeleka ziphiphilitso komanso akalinde ayenela kukhala ndi malangizo a mmene adzacitila zimenezi. N’zosakaikitsa kuti zambili zimene tachulapa mwacita kale. Timakonzekela m’njila yotelo cifukwa cakuti timayamikila mphamvu yopulumutsa ya dipo imeneyi.—1 Pet. 1:8, 9.
3. Kodi tingakonzekeletse bwanji mitima yathu kaamba ka Mgonelo wa Ambuye?
3 Kukonzekeletsa Mitima: N’cinthu cofunika kwambili kukonzekeletsa mitima yathu kuti timvetse tanthauzo la Cikumbutso. (Ezara 7:10) Kuti ticite zimenezi tiyenela kupatula nthawi yosinkha-sinkha Malemba amene asankhidwa kuti tiŵelenge panyengo ya Cikumbutso ndi kuganizila za masiku omaliza a umoyo wa Yesu padziko lapansi. Kuganizila za mzimu wodzipeleka wa Yesu kudzatilimbikitsa kuti tim’tsatile.—Agal. 2:20.
4. Kodi ndi phindu liti maka-maka la dipo limene limakupatsani cimwemwe cacikulu?
4 Imfa ya Kristu imaonetsa kuti Yehova ndi woyenela kulamulila. Imatimasula ku ucimo ndi imfa. (1 Yoh. 2:2) Imatipatsa mwai wokhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso mwai wolandila moyo wosatha. (Akol. 1:21, 22) Imatithandizanso kuti tipitilize kucita zinthu mogwilizana ndi kudzipeleka kwathu kwa Yehova ndi kukhalabe olimba monga ophunzila a Kristu. (Mat. 16:24) Conco lekani kuti cimwemwe canu cipitilize kuonjezeka pamene mukonzekela Cikumbutso ndi kupezekapo!