Ndandanda ya Mlungu wa March 18
MLUNGU WA MARCH 18
Nyimbo 120 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 20 ndime 8-15, ndi bokosi pa tsa. 161 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Luka 1–3 (Mph. 10)
Na. 1: Luka 1:24-45 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Ndani ali Oyenela Kudya Mkate ndi Vinyo pa Mgonelo wa Ambuye?—rs tsa. 72 ndime 3-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mwambo Wokumbukila Imfa ya Yesu Uyenela Kucitika Liti Ndiponso Kangati?—rs tsa. 73 ndime 2-tsa. 74 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 118
Mph. 12: “Alandileni!” Mafunso ndi Mayankho. Citani citsanzo ca mbali ziŵili, mbali yoyamba yoonetsa wofalitsa akulandila mlendo, ndiyeno mbali yaciŵili yoonetsa pambuyo pa msonkhano, wofalitsayo mwaluso akupanga makonzedwe akuti akulitse cidwi mwa mlendoyo.
Mph. 18: “Mmene tingagwilitsile nchito kabuku kakuti Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?” Mafunso ndi Mayankho. Citani citsanzo ca mphindi 7 coonetsa wofalitsa akambitsilana ndi wophunzila Baibo phunzilo limodzi m’kabuku kameneka.
Nyimbo 20 ndi Pemphelo