Ndandanda ya Mlungu wa October 14
MLUNGU WA OCTOBER 14
Nyimbo 32 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jl phunzilo 11 mpaka 13 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Afilipi 1 mpaka Akolose 4 (Mph. 10)
Na. 1: Afilipi 3:17 mpaka 4:1-9 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi N’zoyenela Kusiya Cipembedzo Cimene Munabadwila?—rs tsa. 85 ndime 2 mpaka 4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Pemphelo Lingatithandize Bwanji Kuthana Ndi Mayeselo?—Luka 11:9-13; Yak. 1:5 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 68
Mph. 15: Umodzi Wathu Wapadziko Lonse Umalemekeza Yehova. Nkhani yocokela m’buku la Gulu, tsamba 165, ndime 2, mpaka tsamba 168. Pemphani ena m’gulu kuti afotokoze zocitika mu utumiki zimene anaŵelenga m’zofalitsa zathu zimene zimaonetsa mmene umodzi ndi cikondi ca Mboni za Yehova cinathandizila kucitila umboni.
Mph. 15: “Tidzagaŵila kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38 mu November.” Mafunso ndi Mayankho. Gaŵilani aliyense m’gulu kapepala kamodzi ka Uthenga wa Ufumu Na. 38. Pemphani woyang’anila nchito kuti afotokoze makonzedwe amene alipo ogaŵila kapepala ka uthenga m’gawo lanu. Mwa kugwilitsila nchito ulaliki wacitsanzo uli patsamba 4, onetsani mmene tingagaŵile kapepala ka Uthenga wa Ufumu.
Nyimbo 53 ndi Pemphelo