LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 10/13 tsa. 4
  • Maulaliki Acitsanzo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Maulaliki Acitsanzo
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 10/13 tsa. 4

Maulaliki Acitsanzo

Uthenga wa Ufumu Na. 38

“Tili panchito yapadela imene ikucitika padziko lonse lapansi yogaŵila kapepala ka uthenga wofunika. Ndakubweletselani kanu aka.”

[Muyenela kulankhula mwacidule kuti mumalize gawo lonse. Komabe, nthawi zina mwininyumba angaonetse cidwi ndipo angafune kuti mukambilane naye. Ngati n’conco, mungam’funse kuti afotokoze malingalilo ake pa funso lili patsamba loyamba ndi kumuŵelengela yankho la m’Baibo imene ili mkati mwa kapepala. Ngati nthawi ilola, kambilanani naye mbali zina za kapepala. Musanacoke, muonetseni funso ili patsamba lothela pansi pa mau akuti “Ganizilani Funso Ili” ndi kupangana kuti mukabwelenso kudzakambilana naye.]

Nsanja ya Mlonda November 1

“M’kuona kwanu, kodi muganiza kuti ndi bodza lalikulu liti limene Mulungu wanamizilidwa? [Yembekezani kuti ayankhe.] Baibo imanena kuti Mulungu afuna kuti anthu azim’konda ndi kum’dalila. [Ŵelengani Yesaya 41:13.] Magazini iyi ivumbula mabodza atatu onena za Mulungu amene acititsa kuti anthu ena alephele kumuyandikila.”

Galamukani! November

“Tikufuna kucezako nanu mwacidule kuti timveko malingalilo anu popeza kuti anthu ambili amada nkhaŵa cifukwa ca kusintha kwa khalidwe la anthu. Kodi muganiza kuti khalidwe la anthu likuipila-ipila? [Yembekezani kuti ayankhe.] Baibo linanenelatu kuti khalidwe la anthu lidzasintha. [Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1-5.] Magazini iyi ifotokoza cifukwa cake tiyenela kudalila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani