Ndandanda ya Mlungu wa October 28
MLUNGU WA OCTOBER 28
Nyimbo 31 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jl phunzilo 17 mpaka 19 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: 1 Timoteyo 1 mpaka 2 Timoteyo 4 (Mph. 10)
Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 61
Mph. 5: “Kodi Mudzacita Ciani Pamaholide?” Nkhani.
Mph. 10: Fotokozani Phindu la Uthenga Wabwino. Nkhani yokambilana yocokela m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 159. Citani citsanzo coonetsa mmene tingagaŵilile buku la Baibo Imaphunzitsa mogwilitsila nchito nkhani imene ingakope cidwi ca anthu m’gawo lanu.
Mph. 15: Cifukwa Cake Kusunga Nthawi N’kofunika. Kukambilana. (1) Kodi ndi motani mmene Yehova alili citsanzo cabwino pa nkhani yosunga nthawi? (Hab. 2:3) (2) Kodi kufika kwathu mofulumila pamisonkhano ndi pokonzekela ulaliki kumaonetsa bwanji kuti timalemekeza Yehova ndi kuti timaganizila ena? (3) Kodi kagulu ka ulaliki ndi otsogoza amakhudzidwa bwanji ngati tacedwa kufika pamakambitsilano a ulaliki? (4) N’cifukwa ciani n’kofunika kusunga nthawi tikapangana ndi munthu wacidwi kapena wophunzila Baibo? (Mat. 5:37) (5) Kodi ndi malangizo ati amene angatithandize kuti tizisunga nthawi tikapangana ndi munthu mu ulaliki ndi popita kumisonkhano ya mpingo?
Nyimbo 68 ndi Pemphelo