Ndandanda ya Mlungu wa November 4
MLUNGU WA NOVEMBER 4
Nyimbo 116 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jl phunzilo 20 mpaka 22 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Tito 1 mpaka Filimoni (Mph. 10)
Na. 1: Tito 2:1-15 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Mumaona Kuti N’zoyenela Kukhala M’cipembedzo Cinacake?—rs tsa. 87 ndime 2 mpaka tsa. 88 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa Ciani Sitiyenela ‘Kumvetsela Nkhani Zonama’?—1 Tim. 1:3, 4; 2 Tim. 4:3, 4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 95
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu November. Kukambilana mogwilitsila nchito mafunso otsatilawa: Ngati n’kotheka, cifukwa ciani tiyenela kugaŵilanso magazini pamene tigaŵila tumapepala twa Uthenga wa Ufumu Na. 38 kumapeto kwa mlungu? Ndi liti pamene tingacite zimenezi? Kodi tingakambe ciani pogaŵila magazini pambuyo pakuti tagaŵila kapepala ka Uthenga wa Ufumu? Citani citsanzo coonetsa mmene magazini iliyonse ingagaŵilidwe pamodzi ndi kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Mau a Mulungu ndi Amphamvu. (Aheb. 4:12) Kukambilana kocokela mu buku lapacaka la Mboni za Yehova la 2013, tsamba 57 ndime 1, mpaka tsamba 59, ndime 3. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene aphunzilapo.
Nyimbo 114 ndi Pemphelo