Ndandanda ya Mlungu wa March 24
MLUNGU WA MARCH 24
Nyimbo 104 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 6 ndime ¶7-12, ndi bokosi patsamba 73 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Genesis 47-50 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 48:17 mpaka 49:7 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Zocitika Zosonyeza Kukhalapo kwa Kristu Zimatenga Nyengo ya Zaka Zambili—rs tsa. 162 ndime 1-2 (Mph. 5)
Na. 3: Kudzikuza Kumabweletsa Mavuto (Miy. 11:2; 1 Pet. 5:5-7) (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 56
Mph. 10: Tsatilani Citsanzo ca Nehemiya. Kukambitsilana. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene akuphunzila pa citsanzo ca Nehemiya monga alaliki.
Mph. 10: Gwilitsilani Nchito Mafunso Kuti Muphunzitse Mogwila Mtima—Mbali 1. Nkhani yokambitsilana yocokela m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 236, mpaka tsamba 237, ndime 2. Citani citsanzo cacidule cosonyeza mfundo imodzi ya m’nkhani.
Mph. 10: Yehova Amamvetsela Mapemphelo a Olungama. (1 Pet. 3:12) Nkhani yokambitsilana yocokela mu Buku Lapacaka la 2013, tsamba 66, ndime 1-3; ndi masamba 104 mpaka 105. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene aphunzilapo.
Nyimbo 6 ndi Pemphelo