Mufunika Kubwelelako Mwamsanga
Kucokela nthawi imene Webu saiti yathu inakonzedwanso, anthu opempha phunzilo la Baibulo pa Intaneti akuculukilaculukila. Kuonjezela pamenepo, ulaliki wapoyela watsopano naonso wacititsa kuti anthu ofuna kuphunzila aonjezeke. Pempho lililonse limene lapelekedwa, ofesi ya nthambi imagwililapo nchito mwamsanga. Mwacitsanzo, ngati pempho limenelo lili pa jw.org, akulu a m’gawo la munthu wacidwiyo nthawi zambili ndi amene amalandila cidziŵitso kucokela ku ofesi ya nthambi pakangopita masiku aŵili. Komabe, malipoti akuonetsa kuti ena amene amapempha phunzilo la Baibulo sanafikilidwe kwa milungu ingapo. Conco, tingacite ciani kuti cidwi cake cisanathe, munthuyo tim’thandize?—Maliko 4:14, 15.
Ngati munthu amene sakhala m’gawo lanu aonetsa cidwi, mwamsanga lembani fomu ya Kaonaneni ndi Wacidwi Uyu (S-43) ndi kupatsa kalembela pa msonkhano wanu wotsatila. Ndiyeno kalembela wa mpingo afunika kupeleka cidziŵitso cimeneci ku mpingo woyenelela kapena ku ofesi ya nthambi pasanathe tsiku limodzi kapana aŵili pogwilitsila nchito adilesi ya mpingo pa jw.org. Mipingo imene sikugwilitsila nchito jw.org iyenela kutsatila malangizo amene ali kuseli kwa (S-43). Nthawi zonse akulu afunika kumaonapo pa Webu saiti. Ngati alandila cidziŵitso cakuti afikile munthu winawake, ayenela kupitako mwamsanga kukaonana naye. Wofalitsa aliyense amene wapemphedwa kukaonana ndi munthu wacidwi, ayenela kuona kuti wapatsidwa udindo wofunika kwambili. Ngati munthuyo sanapezeke panyumba, mwina mungasiye zonse zokhudza inuyo monga kumene mukhala, nambala ya foni ndi zina zotelo.