Gwilitsilani Nchito Webusaiti Yathu mu Ulaliki—“Kuyankha Mafunso a m’Baibulo”
Pa jw.org pali cigawo cakuti “Bible Teachings” cimene cili ndi mbali yakuti, “Bible Questions Answered.” Kudziŵa bwino nkhani zimene anthu amakonda kufunsa kaŵilikaŵili, kudzatithandiza kuti tionetse Webusaiti yathu kwa eninyumba amene ali ndi cidwi ndi colinga coti apeze mayankho a m’Malemba pa funso limene angafunse. Tingagwilitsilenso nchito mafunso amenewa poyambitsa makambilano mu ulaliki. Tingayambe ndi funso limene limacititsa cidwi anthu ambili m’gawo lathu, kenako tingapemphe mwininyumba kuti akambe maganizo ake ndi kumuuza zimene Baibulo limanena pogwilitsila jw.org. Pambuyo pake, mufotokozeleni kapena muonetseni kumene mwapeza mayankho. Njila ina ndi kumulola kuti aŵelenge yekha yankho pa Webusaiti. Mkazi wa woyang’anila woyendela wina wakhala ndi zotsatilapo zabwino mwakunena kuti: “Anthu ambili amadabwa kuti, kodi Mulungu ndi amene amacititsa mavuto a anthu?’ Kodi mungakonde kudziŵa yankho lake m’masekondi 51 cabe?” Kenako amapempha munthuyo kuti amvetsele yankho limene anatenga pa intaneti ndi kuika pa pafoni. Iye amamaliza mwa kufotokoza nkhani 11 m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa.