Gwilitsilani Nchito Webusaiti ya jw.org mu Ulaliki—“Khala Bwenzi la Yehova”
Pa webusaiti ya jw.org pali cigawo cakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa” cimene cili ndi mbali ya ana yakuti: “Khala Bwenzi la Yehova.” Cilinso ndi zinthu monga nyimbo, mavidiyo, ndi zocitika. Kodi inuyo munagwilitsilapo nchito cigawo cimeneci mu ulaliki? Ngati mukuphunzila Baibulo ndi makolo amene ali ndi ana ang’ono, bwanji osawasonyeza mbali ya webusaiti imeneyi? Zimenezi zingapangitse kuti io adziŵe mbali zina za webusaiti yathu.
Mwacitsanzo, m’bale wina anagaŵila kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38 kwa mai wina amene anayamba kuŵelenga kapepalako atangokalandila. Mai ameneyo anali ndi ana aang’ono angapo amene anacita cidwi kwambili ndi kapepalako. M’baleyo anafotokozela maiyo mwacidule mfundo zam’kapepalako ndi kumudziŵitsa za adilesi ya Webusaiti yathu imene ili kumbuyo kwa kapepalako. Popeza kuti mai ameneyo anali ndi cidwi kwambili, m’baleyo anaonetsa maiyo ndi ana ake kavidiyo kamodzi ka Kalebe pa foni yake.
Mlongo wina anafotokozela mnzake wa kunchito amene ali ndi ana aang’ono za Webusaiti yathu ndi nkhani zokhudza mabanja zimene zimapezekapo. Mai ameneyu ndi ana ake anatsegula webusaiti ya jw.org. Pambuyo pake, maiyo anauza mlongo wathu kuti ataonelela tumavidiyo twa “Khala Bwenzi la Yehova,” ana ake anayamba kuimba nyimbo yakuti “Lalikira Mawu” uku akuyendayenda m’nyumba.
Inunso idziŵeni bwino mbali imeneyi ya pa jw.org, ndipo tengani mavidiyo, nyimbo kapena zocitika ndi kuziika pa foni yanu. Mukacita zimenezi mudzakhala wokonzeka kugwilitsila nchito cigawo cimeneci ca pa jw.org mu ulaliki. Webusaiti imeneyi ndi cida cabwino kwambili cotithandiza kutumikila Ambuye monga akapolo.—Mac. 20:19.