Ndandanda ya Mlungu wa July 14
MLUNGU WA JULY 14
Nyimbo 1 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 11 ndime 1 mpaka 8 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Levitiko 21-24 (Mph. 10)
Na. 1: Levitiko 23:1-14 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Zoti Anthu Onse Adzapulumuka Si za M’malemba—rs tsa. 94 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Muzigwilitsila Nchito Mwanzelu Nthawi Yovomelezeka Imene Muli Nayo Potumikila Mulungu—2 Akor. 6:2; Aheb. 3:7, 8 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 45
Mph. 10: Konzekelani Kugwila Nchito Yapadela mu August. Gaŵilani aliyense amene alibe kapepala katsopano kakuti, Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo? Citani zitsanzo ziŵili pogwilitsila nchito maulaliki acitsanzo amene ali pa tsamba 4. Citsanzo coyamba cionetse mmene tingagaŵile kapepalako kwa anthu osiyanasiyana. Citsanzo caciŵili cionetse mmene tingakagaŵile kwa munthu amene waonetsa cidwi ndi kuonetsa kuti akufuna kudziŵa zoonjezeleka. Limbikitsani onse kuti akatengemo mbali mokwanila pogwila nchito yapadela imeneyi.
Mph. 5: Pindulani ndi Kuphunzila Malemba Tsiku ndi Tsiku. Kukambilana. Pemphani omvela kuti anene nthawi imene amakambilana lemba la tsiku ndiponso anene mmene kugwilitsila nchito kabuku ka Kuphunzila Malemba Tsiku ndi Tsiku kwawapindulitsila.
Mph. 15: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano N’colinga Cakuti Ticite Ulaliki Wamwai.” Kukambilana. Mucitenso citsanzo.
Nyimbo 107 ndi Pemphelo