Ndandanda ya Mlungu wa September 8
MLUNGU WA SEPTEMBER 8
Nyimbo 133 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 13 ndime 8 mpaka 13 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Numeri 22-25 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 22:36 mpaka 23:1-10 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Satana Si Maganizo Oipa Cabe Amene Anthu Angakhale Nao—rs tsa. 353 ndime 2-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Adamu Analengedwa m’Cifanizilo ca Mulungu m’Njila Iti?—(Gen 1:26) (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 94
Mph. 15: Sonyezani Khalidwe Labwino mu Ulaliki. (2 Akor. 6:3) Gwilitsani nchito mafunso otsatilawa pokambilana: (1) N’cifukwa ciani tiyenela kusonyeza makhalidwe abwino tikamalalikila? (2) Tingasonyeze bwanji makhalidwe abwino (a) gulu lathu likafika m’gawo limene timalalikila? (b) tikamayenda nyumba ndi nyumba? (c) tikaima pakhomo la mwininyumba? (d) mnzathu akamalalikila? (e) mwininyumba akamalankhula? (f) tikapeza mwininyumba wotangwanika kapena ngati nyengo sili bwino? (g) ngati mwininyumba ndi wamwano?
Mph. 15: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelelako.” Nkhani yokambilana. Mukhalenso ndi citsanzo coonetsa wofalitsa akukamba yekha pokonzekela utumiki wakumunda. Pokonzekelapo, iye akukonza funso lakuti akafunse mwininyumba akadzavomela kutenga magazini.
Nyimbo 68 ndi Pemphelo