Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Tikapeza munthu wacidwi, timafuna kubwelelako pa nthawi imene iye amapezeka pa nyumba kuti tikathilile mbeu ya coonadi imene tinafesa. (1 Akor. 3:6) Kuti maziko a ulendo wobwelelako ayalidwe, tiyenela kupempha mwininyumba tisanacoke za tsiku limene tingabwelenso. Kuonjezela pamenepo, zimakhala bwino kusiya funso limene tidzakambilana ulendo wotsatila. Kucita zimenezi kudzacititsa mwininyumba kufunitsitsa kuti tikabwelenso, ndipo ngati yankho la funso limenelo lili m’cofalitsa cimene tamusiyiila, adzakhala wofunitsitsa kuciŵelenga. Kuyala maziko a ulendo wobwelelako, kumacititsa kuti tisavutike kubwelelako cifukwa nkhani imene tidzakambilana imakhala yasankhidwa kale, ndipo mwininyumba amadziŵilatu zimene tidzakambilana. Tikadzaonananso naye tingamuuze kuti tabwela kudzayankha funso limene tinasiya ulendo watha kenako kupitiliza makambilano.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Pokonzekela ulaliki wanu mwezi uno, konzekelaninso funso loti mudzayankhe ulendo wotsatila. Mungauzeko ofalitsa amene mugwila nao nchito funso limene mwakonza.