Ndandanda ya Mlungu wa September 15
MLUNGU WA SEPTEMBER 15
Nyimbo 105 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 13 ndime 20 mpaka 26 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Numeri 26-29 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 27:15–28:1-10 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mulungu Sanalenge Mdyelekezi—rs tsa. 354 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kuopsa kwa Chimo—bh tsa 63 ndime 13-14 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 11
Mph. 15: Kodi Tinacita Zotani? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anila nchito. Fotokozani zimene mpingo wanu unacita m’caka ca utumiki cathaci, kuphatikizapo kampeni yapadela ya mu August. Makamaka fotokozani zinthu zimene unacita bwino, ndipo uyamikileni. Pemphani omvela kuti afotokoze zocitika mu utumiki zilizonse zabwino zimene anakhala nazo mu August, ndipo funsani wofalitsa amene anaonjezela utumiki m’mweziwo. Chulani mfundo imodzi kapena ziŵili zokhudza utumiki zimene mpingo wanu uyenela kuongolela m’caka cautumiki cimene taloŵaci. Fotokozaninso zimene zingathandize mpingo wanu kuongolela mbali zimenezi.
Mph. 15: “Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Nahumu.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 46 ndi Pemphelo