LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 9/14 tsa. 2
  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Nahumu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Nahumu
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mudziŵa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 9/14 tsa. 2

Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Nahumu

1. N’ciani cimene tikuphunzila m’buku la Nahumu?

1 Mabwinja a mzinda wakale wa Nineve amapeleka umboni monga mmene Nahumu analoselela kuti Yehova amalanga adani Ake, ndi kuti ngakhale adaniwo atakhala oopsa bwanji sangathe kulimbana Naye. (Nah. 1:2, 6) Kupenda mosamala ulosi wa Nahumu kungatithandize mu ulaliki.

2. Tingatani kuti uthenga wathu ukhale wolimbikitsa?

2 Pelekani Citonthozo ndi Ciyembekezo: Munthu akangoŵelenga mwacisawawa buku la Nahumu, angaone monga muli cabe uthenga wacionongeko wokhudza Nineve, likulu la mzinda wakale wa anthu onyada wa Asuri. (Nah. 1:1; 3:7) Koma anthu a Yehova anakondwela atamva uthengawu. Nahumu, yemwe dzina lake limatanthauza “Wotonthoza,” analimbikitsa Ayuda anzake kuti posacedwapa mdani wao sadzakhalakonso. M’kupita kwa nthawi, Nahumu anatsimikizila kuti Yehova ndi “malo acitetezo pa tsiku la nsautso.” (Nah. 1:7) Tikamalalikila, ifenso timakhala tikugawana ndi ena uthenga wabwino ndi kuwalimbikitsa kupeza citetezo mwa Yehova.—Nah. 1:15.

3. Tingatengele bwanji citsanzo ca Nahumu pogwilitsila nchito zitsanzo ndi mafanizo?

3 Muzigwilitsila Nchito Zitsanzo ndi Mafanizo: Yehova anauzila Nahumu kuona kufanana kumene kunalipo pakati pa mapeto a Nineve ndi kuonongedwa kwa mzinda wa Iguputo wa ku Thebesi (No-amoni) umene unaonongedwa ndi Asuri. (Nah. 3:8-10) Tikamalankhula ndi anthu za kutha kwa dongosolo loipali la zinthu, tingawauze maulosi a m’Baibulo amene aonetsa kuti Yehova amakwanilitsa mau ake mpaka pa mapeto. Mwacitsanzo, pamene Ababulo ndi Amedi anali kumenyana ndi mzinda wa Nineve mu 632 B.C.E., mvula yaikulu inacititsa mtsinje wa Tigirisi kusefukila, n’kugwetsa mbali ya mpanda wolimba wa mzindawo. Zitatelo, mofulumila mzinda wa Nineve unalandidwa monga mmene Yehova ananenela.—Nah. 1:8; 2:6.

4. Tingalankhule bwanji zinthu zomveka mu ulaliki?

4 Muzilankhula Zomveka Komanso Mwacibadwa: M’kalembedwe kake, Nahumu anafotokoza zinthu mwamphamvu ndi mosapita m’mbali. Mfundo zake zinali zomveka bwino. (Nah. 1:14; 3:1) Ifenso tizigwilitsila nchito mau osavuta kumva. (1 Akor. 14:9) Tikafika pa khomo la munthu ulendo woyamba, tizifotokoza momveka bwino colinga cathu. Pophunzila Baibulo ndi anthu, athandizeni kukulitsa cikhulupililo mwa Yehova ndi m’Mau ake ndiponso kuzindikila mmene zimene akuphunzila zikuwakhudzila.—Aroma. 10:14.

5. Ndi citonthozo cotani cimene timapeza mu ulosi wa Nahumu?

5 Nahumu anakhulupilila kwambili kukwanilitsidwa kwa ulosi wa Yehova, ndipo izi timaziona tikamaŵelenga buku lochedwa ndi dzina lake m’Baibulo. Pamene dongosolo la Satana lili pafupi kutha, timapeza citonthozo pa lonjezo la Mulungu limene limati: “Sipadzakhalanso nsautso.”—Nah. 1:9.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani