Ndandanda ya Mlungu wa October 6
MLUNGU WA OCTOBER 6
Nyimbo 18 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 14 ndime 14-19 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Deuteronomo 1–3 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 2:16-30 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Tatsala Pang’ono Kupeza Mpumulo ku Zinthu Zoipa Zimene Satana Amatilimbikitsa Kucita—rs tsa. 356 ndime 3 mpaka tsa. 357 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Kuti Kugonana Konse ndi Chimo?—rs tsa. 179 ndime 1 mpaka tsa. 180 ndime 3 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 24
Mph. 10: Kugaŵila Magazini mu October. Nkhani yokambilana. Yambani ndi citsanzo coonetsa mmene tingagaŵile magazini pogwilitsila nchito maulaliki acitsanzo amene ali pa tsamba lino. Ndiyeno kambilanani mmene citsanzo ciliconse cinalili.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Tinacita Zotani? Nkhani yokambilana. Pemphani ofalitsa kuti afotokoze mmene apindulila pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti, “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako.” Pemphani omvela kuti afotokoze zocitika zabwino za mu ulaliki.
Nyimbo 83 ndi Pemphelo