Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuonetsa Mocitila Phunzilo la Baibulo Pogwilitsila Nchito Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Anthu ambili sadziŵa zimene timatanthauza tikamanena kuti timaphunzila Baibulo kwaulele ndi anthu panyumba zao. Iwo angamaganize kuti mwina afunika kupezeka pa gulu la ophunzila Baibulo kapena kucita kosi inayake. M’malo mongowauza kuti timaphunzila Baibulo, bwanji osawaonetsa mocitila phunzilo? M’mphindi zocepa cabe, muli pakhomo, mungaonetse munthu kuti phunzilo la Baibulo n’losavuta ndipo n’losangalatsa.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Pemphelani kwa Yehova kuti adalitse kuyesayesa kwanu kuti muyambitse phunzilo la Baibulo.—Afil. 2:13.
Mukadzapita mu ulaliki tsiku lina, mukayese kukhazikitsa phunzilo la Baibulo pogwilitsila nchito buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa, kapena kuonetsa vidiyo yakuti Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji?