Kucititsa Maphunzilo a Baibulo Mogwila Mtima
1. Kodi ndi udindo wotani umene ofalitsa amene amacititsa maphunzilo a Baibulo ali nao?
1 Kulibe amene angatumikile Yehova Mulungu popanda “kukokedwa” ndi iye. (Yoh. 6:44) Ngakhale ndi conco, ofalitsa amene amacititsa maphunzilo a Baibulo ayenela kucita mbali yao pothandiza anthu kuyandikila kwa Atate wao wakumwamba. (Yak. 4:8) Kuti zimenezi zitheke, pamafunika kukonzekela. Conco, kungoŵelenga ndime ndi kufunsa cabe mafunso sikokwanila kuti tithandize wophunzila wathu kumvetsa uthenga ndi kupita patsogolo.
2. Kodi kucititsa phunzilo la Baibulo mogwila mtima kungamuthandize bwanji wophunzila?
2 Kuti ofalitsa acititse maphunzilo ogwila mtima ayenela kuthandiza ophunzila ao kucita zotsatila: (1) kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa, (2) kugwilizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, ndi (3) kucita zimene Baibulo limaphunzitsa. (Yoh. 3:16; 17:3; Yak. 2:26) Zingatenge miyezi kuti tithandize munthu kutsatila masitepi amenewa. Ngakhale ndi conco, sitepi iliyonse ingamuthandize kukulitsa ubwenzi wake ndi Yehova ndi kudzipeleka kwa iye.
3. N’cifukwa ciani aphunzitsi ogwila mtima amafunsa mafunso othandiza munthu kufotokoza maganizo ake?
3 Kudziŵa Zimene Wophunzila Baibulo Akuganiza: Kuti tizindikile ngati wophunzila Baibulo wathu akumvetsa ndi kuvomeleza zimene akuphunzila, tiyenela kupewa kulankhula kwambili ndipo tifunika kum’limbikitsa kufotokoza maganizo ake. (Yak. 1:19) Kodi akumvetsa zimene Baibulo limakamba pa nkhani imene tikuphunzila naye? Kodi angafotokoze nkhaniyo m’mau akeake? Kodi akumva bwanji pa zimene waphunzila? Kodi amakhulupilila kuti zimene Baibulo limaphunzitsa n’zothandiza? (1 Ates. 2:13) Kodi amazindikila kuti zimene amaphunzila ziyenela kumucititsa kusintha umoyo wake? (Akol. 3:10) Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tiyenela kum’funsa mwaluso mafunso omuthandiza kufotokoza maganizo ake, ndiyeno tiyenela kumvetsela akamafotokoza.—Mat. 16:13-16.
4. Tingacite ciani ngati munthu amene tikuphunzila naye Baibulo amavutika kumvetsetsa kapena kugwilitsila nchito zimene aphunzila m’Baibulo?
4 Nthawi zambili, zimene amaganiza ndi zizoloŵezi zake zimazika mizu kwambili cakuti zimatenga nthawi kuti azithetse. (2 Akor. 10:5) Nanga bwanji ngati wophunzila wathu savomeleza kapena kugwilitsila nchito zimene timaphunzila naye? Pamafunika kuleza mtima komanso nthawi yoculuka kuti Mau a Mulungu ndi mzimu woyela zigwile nchito mu mtima mwa wophunzila wathu. (1 Akor. 3:6, 7; Aheb. 4:12) Conco, ngati zikumuvuta kumvetsetsa kapena kugwilitsila nchito zimene akuphunzila m’Baibulo, mungacite bwino kuphunzila nkhani ina m’malo momukakamiza. Pamene tipitiliza kuphunzila naye Baibulo moleza mtima ndi mwacikondi, m’kupita kwa nthawi iye angasinthe.