Ndandanda ya Mlungu wa December 22
MLUNGU WA DECEMBER 22
Nyimbo 15 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 2 ndime 21 mpaka 24, bokosi pa tsa. 24 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Yoswa 9-11 (Mph. 10)
Na. 1: Yoswa 9:16-27 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Palibe Mbali ya Munthu Imene Imakhalabe ndi Moyo Munthu Akafa—rs tsa. 321 ndime 6–tsa. 322 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Cifukwa Cake Tiyenela Kukhala pa Ubwenzi Wabwino ndi Yehova Ndiponso Anthu Amene Amamukonda—lv tsa. 26 ndi 27 ndime 4-7, bokosi pa tsamba 29 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Tulutsani “zabwino” m’cuma cabwino cimene mwapatsidwa.—Mat. 12:35a.
Nyimbo 119
Mph. 5: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 25: “Sukulu ya Ulaliki ya 2015 Idzatithandiza Kunola Luso Lathu Lophunzitsa.” Nkhani yokambilana. Ikambidwe ndi woyang’anila Sukulu ya Ulaliki. Woyang’anila sukulu angasankhe ndime zina kuti ziŵelengedwe asanayambe kukambilana ndi gulu. Fotokozani masinthidwe okhudza nkhani Na.1, nthawi ya mfundo zazikulu, ndi malangizo amene woyang’anila sukulu amapeleka. Ŵelengani ndime 7, ndiyeno pambuyo pokambilana ndimeyo, citani citsanzo coonetsa mkulu akutsogoza phunzilo la banja ndipo ali ndi mkazi wake ndi mwana wake. Pocita phunzilo limeneli, mkuluyo agwilitsile nchito nkhani imene ili pa tsamba 14 m’kabuku kakuti, Mfundo za m’Mau a Mulungu. Limbikitsani onse kuti adzapindule mokwanila ndi maphunzilo abwino a m’sukulu imeneyi ndi kugwilitsila nchito bwino buku la Pindulani ndi sukulu ya utumiki wa Mulungu.
Nyimbo 117 ndi Pemphelo