Ndandanda ya Mlungu wa December 29
MLUNGU WA DECEMBER 29
Nyimbo 37 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 3 ndime 1 mpaka10 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Yoswa 12-15 (Mph. 10)
Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Tulutsani “zabwino” m’cuma cabwino cimene mwapatsidwa.—Mat. 12:35a.
Nyimbo 89
Mph. 20: Aphunzitseni Mwapang’onopang’ono Zinthu “Zabwino” Ophunzila Baibulo ndi Ana Okhulupilila. (Mat. 12:35a) Kukambilana. Gwilitsilani nchito malemba otsatilawa, poonetsa zimene ophunzila Baibulo ndi ana okhulupilila ayenela kucita: 1 Akorinto 13:11; 1 Petulo 2:2, 3. Fotokozani tanthauzo la mau akuti, “kulawa” “mkaka umene uli m’Mau a Mulungu,” ndi mmene tingathandizile ophunzila ndi ana athu kucita zimenezi. Fotokozani mfundo imene ili pa Maliko 4:28. (Onani Nsanja ya Mlonda ya December 15, 2014, tsa. 12, ndime 6-8.) Funsani wofalitsa waluso kapena kholo kuti afotokoze mmene anathandizila wophunzila Baibulo kapena mwana kupita patsogolo mwa kuuzimu.—Aef. 4:13-15; onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2014.
Mph. 10: “Gaŵanani ndi Ena ‘Zabwino’ mwa Kukhala Woceleza (Mat. 12:35a).” Kukambilana. Ndi mapindu otani kapena zocitika zotani zimene ena akhala nazo cifukwa cokhala woceleza? Pemphani omvela kuti anene mmene tingakhalile oceleza kwa ena, makamaka amene ali mu utumiki wa nthawi zonse. Nenani makonzedwe a mpingo a kukonza cakudya ca mbale aliyense amene wabwela kudzakamba nkhani ku mpingo.
Nyimbo 124 ndi Pemphelo