LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 2/15 tsa. 3
  • Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 2/15 tsa. 3

Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki

Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki kuyambila mlungu wa February 23, 2015.

  1. Kodi mizinda yothaŵilako ya ku Isiraeli wakale inali kusiyana bwanji ndi malo obisalako zigaŵenga? (Yos. 20:2, 3) [Jan. 5, w10 11/1 tsa. 15 ndime 4-6]

  2. N’cifukwa ciani Yoswa ananena motsimikizila kwambili mau apa Yoswa 23:14, ndipo n’cifukwa ciani tiyenela kudalila kothelatu malonjezo a Yehova? [Jan. 12, w07 11/1 tsa. 26 ndime 19]

  3. N’cifukwa ciani fuko la Yuda linakhala loyamba kulandila dziko limene analigaŵila? (Ower. 1:2, 4) [Jan. 19, w05 1/15 tsa. 24 ndime 5]

  4. N’cifukwa ciyani Baraki anaumilila kuti mneneli wamkazi Debora apite naye limodzi kunkhondo? (Ower. 4:8) [Jan. 19, w05 1/15 tsa. 25 ndime 4]

  5. Kodi dzina limene Gidiyoni anacha guwa la nsembe limene iye anamanga linaonetsa ciani, nanga ife tikuphunzilapo ciani? (Ower. 6:23, 24) [Jan. 26, w14 2/15 mas. 22-23 ndime 9]

  6. Kodi tiphunzilapo ciani pa yankho limene Gidiyoni anapeleka kwa a Efuraimu amene anali kukangana naye? (Ower. 8:1-3) [Feb. 2, w05 7/15 tsa. 16 ndime 4]

  7. Kodi Yefita anali kuganiza zopeleka nsembe ya munthu pamene anali kunena cowinda cake? (Ower. 11:30, 31) [Feb. 9, w05 1/15 tsa. 26 ndime 1]

  8. Malinga ndi kunena kwa Oweruza 11:35-37, n’ciani cinathandiza mwana wamkazi wa Yefita kukwanilitsa lumbilo la atate wake? [Feb. 9, w11 12/15 mas. 20-21 ndime 15-16]

  9. Pamene mu Isiraeli munalibe mfumu ndipo “aliyense anali kucita zimene anali kuona kuti ndi zoyenela,” kodi zimenezi zinalimbikitsa cisokonezo? Fotokozani. (Ower. 17:6) [Feb. 16, w05 1/15 tsa. 27 ndime 8]

  10. Kodi ndi phunzilo lotani lokhudza kulimbikila kupemphela limene tipezapo pa nkhani ya Aisiraeli amene anagonjetsedwa kaŵili konse ndi mtundu wosamvela wa Benjamini? (Ower. 20:14-25) [Feb. 23, w11 9/15 tsa. 32 ndime 1-4]

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani