Lengezani Coonadi Conena za Yesu Modzipeleka
Tikadziŵa njila zolengezela coonadi cokhudza Yesu timalalikila modzipeleka kwambili. Yesu ndi mwala wapakona womwe cikhulupililo coona cinamangidwapo. (Aef. 2:20) Popanda iye, tikanakhala tilibe ciyembekezo ca moyo wosatha. (Mac. 4:12) Conco, ndi pofunika kwambili kuti onse adziŵe malo amene Yesu ali nao pokwanilitsa colinga ca Mulungu. Anthu ambili asoceletsedwa ndi ziphunzitso zonama zimene si za m’malemba. Zomvetsa cisoni n’zakuti, sangalandile madalitso amene Mulungu walonjeza anthu amene ali ndi cikhulupililo mwa Yesu. Kudzipeleka pankhani ya coonadi kudzatisonkhezela kuthandiza anthu oona mtima kudziŵa bwino Yesu, ubale wake ndi Mulungu ndiponso udindo wake pokwanilitsa colinga ca Mulugu. Conco, m’nyengo ino ya Cikumbutso, kodi mudzalengeza coonadi conena za Yesu modzipeleka?