Muzilimbikitsana pa Nchito Zabwino Modzipeleka
Lemba la Aheberi 10:24 limatilimbikitsa kuti, “tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.” Tingalimbikitse abale athu mwa kukhala citsanzo cabwino ndi kulankhula mau oonetsa kuti tili ndi cikhulupililo. Fotokozelani ena mumpingo zocitika zabwino zimene mwakumana nazo mu ulaliki. Iwo afunika kuona kuti mukusangalala potumikila Yehova. Pa nthawi imodzimodziyo, pewani kuwayelekezela mosayenela ndi inu kapena anthu ena. (Agal. 6:4) Yesetsani kupeza njila yolimbikitsila ena pa “cikondi ndi nchito zabwino” osati pa kudziimba mlandu ndi nchito zabwino. (Onani buku la Sukulu ya Utumiki tsa. 158 ndime 4.) Ngati timalimbikitsa cikondi, ndiye kuti tidzatha kucitila ena zabwino mwakuthupi ndiponso polalikila.—2 Akor. 1:24.