LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 3/15 tsa. 1
  • Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Konzekelani Cikumbutso ndi Mtima Wacimwemwe
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Cifukwa Cake Timacita Mgonelo wa Ambuye
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Yehova Amadalitsa Kuyesetsa Kwathu Kuti Ticite Cikumbutso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 3/15 tsa. 1

Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?

Pa Nisani 13 mu 33 C.E, Yesu asanaphedwe, anazindikila kuti watsala ndi usiku umodzi wokhala ndi anzake apamtima. Conco, iye anadziŵa kuti afunika kucita nao mwambo wa Pasika womaliza ndiyeno kuyambitsa mwambo watsopano wa Mgonelo wa Ambuye. Mwacionekele anafunika kukonzekela cocitika capadela cimeneci. Conco, Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane kuti akasonkhanitse zinthu. (Luka 22:7-13) Kuyambila nthawi imeneyo, Akristu amene afuna kucita mwambo wa Cikumbutso caka ndi caka afunika kukonzekela. (Luka 22:19) Ndi zinthu zofunika ziti zimene tingacite pokonzekela Cikumbutso cimene tidzacita pa April 3?

Zimene Akulu Ayenela Kukonzekela:

  • Konzani zoti mugwilitsile nchito Nyumba ya Ufumu kapena malo ena oyenelela. Malowo akhale okwanila bwino, owala bwino, ndiponso okhala ndi mpweya wokwanila. Konzani zakuti mudzayeletse bwinobwino malo amene mudzacitila cikumbutso kukali nthawi.

  • Sankhani mkambi woyenelela, cheyamani ndi abale opeleka pemphelo pa zizindikilo.

  • Ngati mipingo ingapo idzacitila pa malo amodzi, muyenela kukambilana pasadakhale za nthawi ya kuloŵa ndi kutuluka pa malopo, ndiponso malo oikako magalimoto.

  • Sankhani amene adzacita ukalinde ndi amene adzapelekela zizindikilo.

  • Konzani zodzakhala ndi zizindikilo zoyenelela, mbale, matambula a vinyo, thebulo ndiponso nsalu ya pa thebulo.

Zimene Ofalitsa Ayenela Kukonzekela:

  • Konzani zodzagwila nao mokwanila nchito yoitanila anthu ku Cikumbutso.

  • Lembani maina a anthu amene mufuna kudzaitanila ku Cikumbutso. Mungaitane maphunzilo a Baibulo, anzanu a kusukulu, kunchito ndi ena amene mudziŵa.

  • Mudzaŵelenge ndi kusinkhasinkha Malemba oŵelenga pa nyengo ya Cikumbutso.

  • Konzekelani kudzalandila alendo pa Cikumbutso.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani