Ndandanda ya Mlungu wa March 9
MLUNGU WA MARCH 9
Nyimbo 44 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 6 ndime 9-15 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Samueli 1–4 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Samueli 2:30-36 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Baibulo Linalosela Ciani za Mesiya?—igw-CIN tsa.10 (Mph. 5)
Na. 3: Asa—Mutu: Khalani Acangu pa Kulambila Koona—w14 8/15 tsa. 17 ndime 4-6 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: ‘Khalani Okonzeka Kugwila Nchito Iliyonse Yabwino.’—Tito 3:1.
Nyimbo 45
Mph. 10: ‘Khalani Okonzeka Kugwila Nchito Iliyonse Yabwino.’ Nkhani yozikidwa pa lemba la mwezi. Ŵelengani ndi kukambilana Miyambo 21:5, Tito 3:1 ndi 1 Petulo 3:15. Fotokozani mmene kukonzekela bwino kumapindulitsila Akristu. Mwacidule, chulani nkhani za mu Msonkhano wa Nchito za mwezi uno, ndipo fotokozani mmene zikugwilizanilana ndi lemba la mwezi.
Mph. 10: Kufunsa Mafunso Woyang’anila Sukulu ya Ulaliki. Kodi nchito yanu ndi yotani? Nanga mumakonzekela bwanji kuti mucititse sukulu mlungu uliwonse? N’cifukwa ciani ophunzila ayenela kukonzekela bwino mbali zao? Ndi mapindu otani amene omvela angapeze ngati amakonzekela nkhani zonse asanabwele kumisonkhano?
Mph. 10: “Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?” Kukambilana. Mwacidule, fotokozani mfundo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2013 tsamba 2. Ndiyeno citani citsanzo coonetsa wofalitsa akulandila mlendo pa Cikumbutso.
Nyimbo 8 ndi Pemphelo