Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?
Pa Nisani 13 mu 33 C.E, Yesu asanaphedwe, anazindikila kuti watsala ndi usiku umodzi wokhala ndi anzake apamtima. Conco, iye anadziŵa kuti afunika kucita nao mwambo wa Pasika womaliza ndiyeno kuyambitsa mwambo watsopano wa Mgonelo wa Ambuye. Mwacionekele anafunika kukonzekela cocitika capadela cimeneci. Conco, Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane kuti akasonkhanitse zinthu. (Luka 22:7-13) Kuyambila nthawi imeneyo, Akristu amene afuna kucita mwambo wa Cikumbutso caka ndi caka afunika kukonzekela. (Luka 22:19) Ndi zinthu zofunika ziti zimene tingacite pokonzekela Cikumbutso cimene tidzacita pa April 3?
Zimene Ofalitsa Ayenela Kukonzekela:
Konzani zodzagwila nao mokwanila nchito yoitanila anthu ku Cikumbutso.
Lembani maina a anthu amene mufuna kudzaitanila ku Cikumbutso. Mungaitane maphunzilo a Baibulo, anzanu a kusukulu, kunchito ndi ena amene mudziŵa.
Mudzaŵelenge ndi kusinkhasinkha Malemba oŵelenga pa nyengo ya Cikumbutso.
Konzekelani kudzalandila alendo pa Cikumbutso.