UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Kodi Mungayeseko kwa Caka Cimodzi?
Kuyesako ciani? Upainiya wa nthawi zonse. Mudzapeza madalitso ambili mukakhala mpainiya—Miy. 10:22.
KUKHALA MPAINIYA KUDZAKUTHANDIZANI . . .
kukulitsa luso lolalikila, ndipo mudzasangalala kwambili ndi utumiki wanu
kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Mukamauza ena za iye, mudzayamba kuganizila kwambili makhalidwe ocititsa cidwi a Mulungu
kukhala wokhutila cifukwa coika Ufumu patsogolo mu umoyo wanu. Ndipo mudzakhala ndi cimwemwe kaamba ka kudzipeleka kuti muthandize ena. —Mat. 6:33; Mac. 20:35
kukhala ndi mwayi wopezeka pa miting’i ya apainiya pamene woyang’anila dela akucezela mpingo wanu, miting’i yapadela msonkhano wadela usanayambe, ndi kupezeka pa Sukulu ya Apainiya
kukhala ndi mwayi woyambitsa ndi kutsogoza maphunzilo ambili a Baibulo
kukhala ndi nthawi yambili yoceza ndi kulimbikitsana ndi alaliki anzanu. —Aroma 1:11, 12