CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | SALIMO 119
“Muzitsatila Cilamulo ca Yehova”
Kutsatila cilamulo ca Yehova kutanthauza kumvela malangizo a Mulungu ndi mtima wonse. M’Baibulo muli zitsanzo zambili za anthu amene anali kutsatila ndi kudalila cilamulo ca Yehova monga mmene wamasalimo anacitila.
Kutsatila cilamulo ca Mulungu n’kumene kumatipatsa cimwemwe ceni-ceni
119:1-8
Yoswa anali kudalila kwambili malangizo a Yehova. Anadziŵa kuti ngati afuna kukhala wacimwemwe ndi kuti zinthu zimuyendele bwino, anafunika kukhulupilila Yehova na mtima wake wonse
Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tikhale olimba mtima polimbana ndi ziyeso
119:33-40
Yeremiya anaonetsa kuti anali wolimba mtima ndipo anadalila Yehova ngakhale kuti anakumana ndi mavuto. Anapitiliza kukhala na umoyo wosalila zambili ndi kugwila nchito imene anapatsidwa.
Kudziŵa bwino Mawu a Mulungu kumatithandiza kulalikila molimba mtima
119:41-48
Paulo sanacite mantha kuuza aliyense uthenga wocokela kwa Mulungu. Iye anali kukhulupilila kuti Yehova adzamuthandiza kulalikila molimba mtima kwa Bwanamkubwa Felike
Ni pa zocitika ziti pamene ningaonetse kulimba mtima polaliki ena?
Kusukulu
Kunchito
Kwa Acibale
Kwina