LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 3 tsa. 3
  • Mungasangalale na Madalitso Osatha Ocokela kwa Mulungu Wacikondi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mungasangalale na Madalitso Osatha Ocokela kwa Mulungu Wacikondi
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • M’nkhani zotsatila, tikulimbikitsani kuganizila izi:
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Mungapeze Madalitso Osatha kwa Mlengi Wathu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Limbitsani Cikhulupililo Canu mwa Mlengi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 3 tsa. 3
Banja likuceza capamodzi mwacimwemwe. Makolo akhala pampando wa sofa ndipo agwilana manja pamene ana ajambula zithunzi pa thebulo.

Mungasangalale na Madalitso Osatha Ocokela kwa Mulungu Wacikondi

  • Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko limene mulibe nkhondo, ciwawa, na mikangano?

  • Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko lopanda matenda, mavuto, kapena imfa?

  • Kodi mumalakalaka kukhala wopanda nkhawa?

  • Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko lopanda matsoka a zacilengedwe?

Mulungu wathu wacikondi, amene analenga dziko lapansi lokongolali, analonjeza kuti adzadalitsa mtundu wa anthu powapatsa moyo wosatha, komanso wacimwemwe m’dziko lamtendele. Amenewa si maloto cabe.

M’nkhani zotsatila, tikulimbikitsani kuganizila izi:

  • Mmene Mlengi wathu amaonela anthu

  • Zimene Mawu a Mulungu amatiuza

  • Zimene aneneli anakamba ponena za madalitso amene Mulungu analonjeza

  • Zimene tingacite kuti tikhale acimwemwe palipano, na kuti Mulungu akatipatse madalitso osatha kutsogolo

Tiyeni tiyambe na kuona mmene Mlengi wathu amakondela anthu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani