LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 3 tsa. 11
  • Madalitso kwa Anthu Omvela Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Madalitso kwa Anthu Omvela Mulungu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 1. KUMVELA MULUNGU KUMATIPATSA NZELU
  • 2. KUMVELA KUMATIPATSA CIMWEMWE
  • Cikondi Ca Mulungu N’camuyaya
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Izi Ndi Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Kodi Ndinu ‘Wokonzeka Kumvela’?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • ‘Tamvelani Maloto Awa’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 3 tsa. 11
Banja likucitila pamodzi zinthu mosangalala. Mayi ali ku khichini akukonza cakudya na mmodzi wa ana ake. Tate ali m’cipinda cocezela na mwana wina wamkazi ndipo akuyang’ana mapikica.

Tingakhale na cimwemwe ceni-ceni ngati tisunga malamulo a Mulungu

Madalitso kwa Anthu Omvela Mulungu

Mneneli Mose anakamba kuti ngati timvela malamulo a Mulungu, tidzalandila madalitso ake. (Deuteronomo 10:13; 11:27) Timamvela Mulungu osati cifukwa cowopa kuti angatilange. Makhalidwe abwino a Mulungu amatilimbikitsa kumumvela cifukwa timam’konda, ndipo timafuna kupewa kucita ciliconse cimene cingam’khumudwitse. Malemba amati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.”—1 Yohane 5:3.

Kodi tingapeze bwanji madalitso cifukwa comvela Mulungu? Tiyeni tione mfundo ziŵili izi.

1. KUMVELA MULUNGU KUMATIPATSA NZELU

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, . . . kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.”—YESAYA 48:17.

Mlengi wathu Yehova Mulungu amatidziŵa bwino, ndipo amapeleka malangizo amene tifunikila. Ngati tifuna kuti ziphunzitso zake zizitithandiza kupanga zosankha zanzelu, tifunika kumaŵelenga Malemba Oyela kuti tidziŵe zimene Mulungu afuna kuti tizicita, n’kumacitadi zimenezo.

2. KUMVELA KUMATIPATSA CIMWEMWE

“Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—LUKA 11:28.

Masiku ano, pali anthu ofika m’mamiliyoni amene amamvela Mawu a Mulungu ndipo amapeza cimwemwe ceni-ceni. Mwacitsanzo, ganizilani za munthu wina wa ku Spain amene anali na mtima wapacala, komanso wankhanza kwa anthu ena, ngakhale kwa mkazi wake. Tsiku lina, iye anaŵelenga mawu a mneneli Mose okamba za khalidwe la kufatsa kwa Yosefe, mwana wa Yakobo. Yosefe anagulitsidwa monga kapolo, ndipo anam’ponya m’ndende pamlandu wom’semela. Koma ngakhale n’telo, iye anakhalabe wofatsa, wobweletsa mtendele, komanso wokhululuka. (Genesis, macaputala 37-45) Munthu wa ku Spain uja anati: “Citsanzo ca Yosefe cinan’limbikitsa kukulitsa makhalidwe a kufatsa, kukoma mtima, komanso kudziletsa. Ndipo tsopano nili na umoyo wacimwemwe.”

Malemba Oyela amapeleka malangizo otithandiza kudziŵa mmene tiyenela kucitila zinthu na ena. Tiyeni tiimvetse mfundoyi m’nkhani yotsatila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani