CUMA COCOKELA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 29-33
“Mfumu Idzalamulila Mwacilungamo”
Mfumu Yesu, waika “akalonga,” amene ni akulu, kuti asamalile nkhosa
32:1-3
Mofanana ndi “malo ousapo mvula yamkuntho,” akulu amateteza nkhosa ku mazunzo na zinthu zolefula
Mofanana ndi “mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi,” akulu amatsitsimula amene ali na ludzu lauzimu, mwa kuwapatsa coonadi coyela, cosasukuluka
Mofanana ndi “mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma,” akulu amateteza nkhosa mwa kuzipatsa malangizo ndi kuzitsitsimula