UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kusamalila Malo Athu Olambilila
Nyumba zathu za Ufumu si Nyumba wamba; ni malo olambilila opelekedwa kwa Yehova. Kodi aliyense wa ife angathandize bwanji posamalila Nyumba ya Ufumu? Pambuyo potamba vidiyo yakuti Kusamalila Malo Athu Olambilila kambilanani mafunso aya.
Kodi Nyumba za Ufumu zimagwila nchito yanji?
N’cifukwa ciani tiyenela kusunga Nyumba yathu ya Ufumu ili yoyela ndi yokonzedwa bwino?
N’ndani amasamalila nchito yokonza Nyumba ya Ufumu?
N’cifukwa ciani kupewa ngozi n’kofunika? Nanga mu vidiyo mwaonamo zitsanzo zanji zopewela ngozi?
Kodi tingalemekeze bwanji Yehova ndi zopeleka zathu?