CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | ZEKARIYA 9-14
Khalani m’Cigwa ca “Pakati pa Mapili”
14:3-5
Yehova anapanga “cigwa cacikulu kwambili” mu 1914, pamene anakhazikitsa Ufumu wa Mesiya, umene ni “phili” locepelapo pa ulamulilo wake wa cilengedwe conse. Kuyambila mu 1919, atumiki a Mulungu akhala otetezeka m’cigwa ca “pakati pa mapili” cimeneco
Kodi anthu amathaŵila motani ku cigwa ca citetezo?
14:12, 15
Aliyense amene adzakhala kunja kwa cigwa cophiphilitsaco adzawonongedwa pa Aramagedo
Ningacite ciani kuti nikhale m’cigwa ca citetezo?