LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb17 December tsa. 5
  • Mbali Yatsopano pa Msonkhano wa Mkati mwa Wiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mbali Yatsopano pa Msonkhano wa Mkati mwa Wiki
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Amaona Kuti “Ameni” Wanu ni Wofunika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
mwb17 December tsa. 5
Uthenga Wabwino wa Mateyu mu Baibo yophunzilila ya pa intaneti ya Baibulo la Dziko Latsopano.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mbali Yatsopano pa Msonkhano wa Mkati mwa Wiki

Kuyambila mu January 2018, pa misonkhano ya mkati mwa wiki tizikambilananso mfundo zounikila, na zithunzi zocokela mu Baibo yophunzilila ya pa intaneti ya Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika (nwtsty), imene pakali pano tilibe m’Cinyanja. Mosakayikila, mbali yatsopanoyi izikuthandizani kwambili pokonzekela misonkhano. Koma maka-maka, idzakuthandizani kumuyandikila kwambili Yehova, Atate wathu wacikondi.

MFUNDO ZOUNIKILA

Mfundo zounikila zizifotokoza za cikhalidwe, malo, na zinenelo m’mavesi ambili a m’Baibo.

Mateyu 12:20

Nyale Yofuka: Kale, nyale imene anthu ambili anali kuseŵenzetsa inali nsupa, imene anali kuthilamo mafuta a maolivi. Inali kuyaka cifukwa mafuta anali kukwela ku thambo yake. M’cigiriki, mau akuti “nyale yofuka” angatanthauze nthambo ya nyale yofuka utsi cifukwa cakuti moto ukaliko koma lawi lake likuzima kapena lazimilatu. Ulosi wa pa Yesaya 42:3 unakambilatu za cifundo ca Yesu, kuti sadzazimitsa ciyembekezo ca anthu odzicepetsa ndi opondelezedwa.

Mateyu 26:13

Ndithu: Liu la Cigiriki lakuti a·menʹ, lotengedwa ku liu la Ciheberi lakuti ʼa·menʹ, limatanthauza kuti “zoona” kapena “ndithudi.” Nthawi zambili Yesu akafuna kukamba mau ena ake, lonjezo, kapena ulosi, anali kuyamba na mau amenewa. Anali kucita izi pofuna kuonetsa kuti zimene anali kukamba zinalidi zoona. Yesu anali kukonda kuseŵenzetsa mau akuti “ndithu” kapena ameni, m’njila imeneyi m’zolemba zopatulika. Mau a Yesu amenewa akabwelezedwa (ameni, ameni), amamasulidwa kuti “ndithudi” monga mu Uthenga Wabwino wa Yohane.—Yoh. 1:51.

ZITHUNZI

Mapikica, zithunzi-thunzi, tumavidiyo topanda mau, na tukadoli, zonse zionetsa zinthu zambili zolembedwa m’Baibo.

Betefage, Phili la Maolivi, na Yerusalemu

Kavidiyo kameneka kaonetsa njila yocoka kum’maŵa kwa mudzi wochedwa et-Tur kupita ku Yerusalemu. Zioneka kuti mudziwu unali pafupi na Betefage wochulidwa m’Baibo, umene uli pamwamba pa Phili la Maolivi. Mzinda wa Betaniya uli kum’maŵa kwa mzinda wa Betefage, pafupi na Phili la Maolivi. Yesu na ophunzila ake akakhala ku Yerusalemu, nthawi zambili anali kugona ku Betaniya, mzinda umene masiku ano umadziŵika kuti el-ʽAzariyeh (El ʽEizariya ), dzina la Ciarabu lotanthauza “Kwawo kwa Lazaro.” Mosakayika, Yesu anali kufikila kunyumba kwa Marita, Mariya na Lazaro. (Mat. 21:17; Maliko 11:11; Luka 21:37; Yoh. 11:1) Pocoka ku Betaniya kupita ku Yerusalemu, Yesu ayenela kuti anali kupitila njila imene taona mu vidiyo. Pa Nisani 9, mu 33 C.E., Yesu anakwela bulu popita ku Yerusalemu, ndipo anapitila njila yodutsa pa phili la maolivi. Mwacionekele, anapitila njila yocoka ku Betefage kupita ku Yerusalemu.

Njila imene Yesu ayenela kuti anapitila pocoka ku Betaniya kupita ku Yerusalemu
  1. Njila yocoka ku Betaniya kupita ku Betefage

  2. Betefage

  3. Phili la Maolivi

  4. Cigwa ca Kidironi

  5. Kacisi wa pa Phili

Msomali mu fupa la kadendene

Fupa la kadendene ka munthu kokhomedwa msomali

Ici ni cithunzi ca fupa la kadendene ka munthu kokhomeleledwa msomali wotalika 11.5 cm. Fupali linafukulidwa mu 1968 ca kum’poto kwa Yeresalemu, ndipo ndi lakale m’nthawi za Aroma. Limapeleka umboni wakuti misomali anali kuiseŵenzetsa popha munthu mwa kum’khomelela pamtengo. Msomaliwu ungafanane na imene asilikali aciroma anakhomelela Yesu Khristu pa mtengo. Fupa limeneli analipeza m’bokosi lamwala. M’bokosimo anali kusungilamo mafupa ouma a anthu akufa pambuyo pakuti mnofu unawola. Izi zionetsa kuti munthu amene anali kufela pa mtengo anali kuikiwa m’manda.—Mat. 27:35.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani