UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Pewani Kunyada na Mkwiyo
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Yesu anaphunzitsa kuti ophunzila ake adzadziŵika cifukwa ca cikondi. (Yoh. 13:34, 35) Kuti tionetse cikondi monga ca Khristu, tifunika kuika zofuna za ena patsogolo na kupewa kukwiya. —1 Akor. 13:5.
MMENE TINGACITILE:
Ngati munthu wina wakamba kapena kucita zokukwiyitsani, yambani mwaima na kuganizila zimene zam’pangitsa kuti akambe kapena kucita zimenezo. Ganizilaninso zotulukapo za zimene mufuna kucita.—Miy. 19:11
Kumbukilani kuti tonse ndise opanda ungwilo, ndipo nthawi zina tingakambe kapena kucita zinthu zimene pambuyo pake tingadziimbe nazo mlandu
Mukasemphana maganizo, muzithetsa nkhani mwamsanga
TAMBANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—PEWANI KUNYADA NDI KUCITA ZOSAYENELA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi m’bale Larry anaonetsa bwanji kuti sanakondwele na lingalilo la m’bale Tom?
Kodi kuyamba waima kuti aganizilepo kunam’thandiza bwanji mbale Tom kuti apewe kukwiya?
Kodi kuyankha modekha kwa m’bale Tom kunathandiza bwanji?
Kodi mpingo umapindula bwanji ngati tikhalabe odekha wina akatikwiyitsa?