CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 23-24
Apatsidwa Mlandu Wakuti ni Wovutitsa Komanso Woukila Boma
23:12, 16; 24:2, 5, 6, 10-21
Ayuda a ku Yerusalemu ‘analumbila mwa kudzitembelela’ n’colinga cakuti aphe Paulo. (Mac. 23:12) Komabe, colinga ca Yehova cinali cakuti Paulo apite ku Roma kukacitila umboni. (Mac. 23:11) Mwana wamwamuna wa mlongo wake wa Paulo atamva za ciwembuco, anakanena kwa Paulo, pofuna kumuteteza kuti asaphedwe. (Mac. 23:16) Kodi cocitikaci cakuphunzitsani ciani ponena za . . .
amene amayesa kulepheletsa colinga ca Mulungu?
njila imene Mulungu angaseŵenzetse potithandiza?
kulimba mtima?