CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 25-26
Paulo Apempha Kukaonekela kwa Kaisara Kenako Alalikila Mfumu Herode Agiripa
25:11; 26:1-3, 28
Ngakhale kuti sitifunika kuda nkhawa kuti tidzakamba ciani akatipeleka kwa “abwanamkubwa ndi mafumu,” tifunika ‘kukhala okonzeka nthawi zonse kuyankha’ aliyense amene watifunsa za ciyembekezo cathu. (Mat. 10:18-20; 1 Pet. 3:15) Tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo ngati otsutsa “akuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo”?—Sal. 94:20.
Mwa kuseŵenzetsa ufulu wathu wa lamulo poteteza uthenga wabwino.—Mac. 25:11
Mwa kukhala aulemu pokamba na akulu-akulu a boma.—Mac. 26:2, 3
Ngati m’poyenela, mwa kufotokoza mmene uthenga wabwino watipindulitsila na mmene wapindulitsila ena.—Mac. 26:11-20