UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kupatsidwa Ufulu Wolalikila ku Quebec
Pa nthawi imene Paulo anali kuimbidwa mlandu, anapempha kuti akaonekele kwa Kaisara. Poseŵenzetsa ufulu wake monga nzika ya Roma, iye anatipatsa citsanzo cabwino cofunika kutengela masiku ano. Tambitsani vidiyo yakuti “Kupatsidwa Ufulu Wolalikila ku Quebec,” kuti tidziŵe mmene abale anaseŵenzetsela ufulu wa lamulo poteteza uthenga wabwino ku Quebec. Pambuyo pake, yankhani mafunso aya:
Kodi abale athu ku Quebec anakumana na mavuto otani?
Ni kathirakiti kati kapadela kamene iwo anagaŵila? Nanga panakhala zotulukapo zanji?
N’ciani cinacitikila M’bale Aimé Boucher?
Kodi Khoti Lalikulu ku Canada linagamula ciani pa mlandu wa M’bale Boucher?
Ni ufulu wa lamulo uti umene suseŵenza kaŵili-kaŵili umene abalewa anauseŵenzetsa? Nanga panakhala zotulukapo zabwanji?
N’ciani cinacitika pambuyo pakuti apolisi motunthiwa na ansembe aimitsa misonkhano yampingo?