UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mungaphunzile Ciani kwa Iwo?
Kodi ndinu mkulu kapena mtumiki wothandiza watsopano? N’kutheka kuti muli na maluso, mphatso, kapena munapata maphunzilo a kuthupi kuposa akulu na atumiki othandiza ena mu mpingo mwanu. Ngakhale n’conco, pali zambili zimene mungaphunzile kwa abale amene ali m’bungwe la atumiki. Mungaphunzilenso zambili kwa amuna okhulupilika amene satumikilanso m’bungweli cifukwa ca zovuta zina monga ukalamba, thanzi, kapena cifukwa ca maudindo a m’banja.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MUZILEMEKEZA ACIYAMBAKALE, PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AYA:
1. Kodi M’bale Richards anaonetsa bwanji kuti amalemekeza M’bale Bello?
2. Kodi m’bale Ben analakwitsa ciani? Nanga n’cifukwa ciani?
3. Kodi Ben anaphunzilapo ciani pa citsanzo ca Elisa?
4. Kaya ndinu m’bale kapena mlongo, kodi mungaonetse bwanji kuti mumalemekeza Akhristu amene ni aciyambakale? Nanga mungacite ciani kuti muphunzile kwa iwo?