MUTU 6
Atumiki Othandiza Amacita Utumiki Wofunika
M’KALATA yake ku mpingo wa ku Filipi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ine Paulo ndili pamodzi ndi Timoteyo monga akapolo a Khristu Yesu. Ndikulembela oyela onse ogwilizana ndi Khristu Yesu amene ali ku Filipi, komanso oyang’anila ndi atumiki othandiza.” (Afil. 1:1) Onani kuti iye anapelekanso moni kwa atumiki othandiza. N’zoonekelatu kuti amuna amenewa anali kucita gawo lofunika lothandizila akulu mumpingo pa nthawiyo. N’cimodzimodzinso masiku ano. Atumiki othandiza amagwila nchito zothandiza oyang’anila kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo mumpingo.
2 Kodi atumiki othandiza mumpingo wanu muwadziŵa? Kodi mudziŵa nchito zimene amagwila popindulitsa imwe na mpingo wonse? Mosakayika konse, Yehova amayamikila nchito za amuna amenewa. Paulo analemba kuti: “Amuna otumikila bwino amakhala ndi mbili yabwino ndi ufulu waukulu wa kulankhula za cikhulupililo, mwa Khristu Yesu.”—1 Tim. 3:13.
ZIYENELEZO ZA M’MALEMBA ZA ATUMIKI OTHANDIZA
3 Mtumiki wothandiza amayembekezedwa kukhala Mkhristu wacitsanzo cabwino, wodalilika, komanso wosamalila bwino nchito zake. Mtumwi Paulo anaonetsa bwino zimenezi pokamba pa ziyenelezo zawo, m’kalata imene analembela Timoteyo. Iye analemba kuti: “Nawonso atumiki othandiza akhale opanda cibwana, osanena paŵili, osakonda kumwa vinyo wambili, ndiponso osakonda kupeza phindu mwacinyengo. Akhale ogwila cikhulupililo mwamphamvu, cimene ndi cisinsi copatulika ca Mulungu, ali ndi cikumbumtima coyela. Ndiponso, amenewa ayesedwe kaye ngati ali oyenelela, ndiyeno atumikile monga atumiki, popeza ndi opanda cifukwa cowanenezela. Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi, oyang’anila bwino ana awo ndi mabanja awo.” (1 Tim. 3:8-10, 12) Kuonetsetsa kuti atumiki othandiza akusunga muyezo wapamwamba umenewu kumateteza mpingo kuti usanenezedwe kuti umapeleka maudindo kwa anthu osayenelela.
4 Mwezi uliwonse, atumiki othandiza acikulile na acicepele omwe, ayenela kutengako mbali mwakhama mu ulaliki. Potengela citsanzo ca Yesu, iwo amakhala okangalika pa ulaliki. Mwakutelo, amaonetsa kuti nawonso amafuna kuti anthu akapulumuke, mmene Yehova akufunila.—Yes. 9:7.
5 Atumiki othandiza ayenela kukhalanso acitsanzo cabwino pa mavalidwe, kudzikongoletsa, malankhulidwe, maganizo, komanso pa khalidwe lawo. Ayenela kukhala oganiza bwino kuti ena aziŵalemekeza. Kuwonjezela apo, satenga mopepuka ubale wawo na Yehova, ngakhale utumiki wawo mumpingo.—Tito 2:2, 6-8.
6 Amuna amenewa amayamba ‘ayesedwa kuona ngati ali oyenelela.’ Ngakhale asanaikidwe pa udindowu amakhala akuonetsa kale kuti ni amuna odzipeleka mofikapo. Amaonetsa kuti amaika zinthu za Ufumu patsogolo mu umoyo wawo, ndipo akukalamila utumiki uliwonse umene angapatsidwe. Amakhaladi zitsanzo zabwino zimene ena angatengeleko mumpingo.—1 Tim. 3:10.
NCHITO ZA ATUMIKI OTHANDIZA
7 Atumiki othandiza amagwila nchito zolekana-lekana potumikila abale na alongo. Izi zimapatsa oyang’anila nthawi yokwanila yosamalila maudindo a kuphunzitsa komanso ubusa. Bungwe la akulu popatsa atumiki othandiza zocita, limaona maluso a wina aliyense payekha-payekha komanso zofunikila za mpingo.
Atumiki othandiza amagwila nchito zolekana-lekana. Izi zimapatsa oyang’anila nthawi yokwanila yosamalila maudindo a kuphunzitsa komanso ubusa.
8 Nazi zina mwa nchito za atumiki othandiza: Mtumiki wothandiza wina angapatsidwe nchito yosamalila mabuku kuti tizipeza mabuku athu oŵelenga, komanso oseŵenzetsa mu ulaliki. Ena angapatsidwe nchito yosamalila maakaunti a mpingo kapena makhadi a magawo. Enanso angapatsidwe yosamalila mamaikolofoni, ena kusaundi, ena kukhala akalinde, ndiponso kuthandiza akulu m’njila zolekana-lekana. Palinso nchito zambili zosamalila Nyumba ya Ufumu kuti ikhale yosamalika bwino komanso yaukhondo. Conco, nthawi zambili atumiki othandiza amapemphedwa kuti asamalile mbali zimenezi.
9 M’mipingo ina, zimatheka kugaŵila nchito imodzi kwa mtumiki wothandiza aliyense. Koma m’mipingo ina, mtumiki wothandiza mmodzi angapatsidwe nchito zingapo. M’mipingo inanso, atumiki othandiza aŵili kapena oposelapo angapatsidwe nchito imodzi. Ngati atumiki othandiza si okwanila kuti asamalile maudindo ena, bungwe la akulu lingasankhe abale obatizika acitsanzo cabwino kuti asamalile nchitozo. Adzakhala na cidziŵitso pa nchitozo cimene cidzaŵathandiza kutsogolo akadzayenelezedwa kukhala atumiki othandiza. Ngati palibiletu abale oyenelela, mlongo wacitsanzo cabwino angapemphedwe kuthandizako nchito zina, ngakhale kuti sangaikidwe kukhala mtumiki wothandiza. Munthu wacitsanzo cabwino, ni uja amene ena angatengeleko citsanzo cake pa makhalidwe ake komanso pa nkhani ya kulambila. Ena ayenela kutengela citsanzo kwa iye pa nkhani ya kupezeka kumisonkhano, kutengako mbali mu ulaliki, umoyo wabanja, zosangalatsa zimene amasankha, mavalidwe na kudzikongoletsa, na zina zotelo.
10 M’mipingo yokhala na akulu ocepa kwambili, atumiki othandiza ocita bwino angapatsidweko mbali yopenda ofalitsa ofunsila ubatizo. Koma azikambilana nawo cabe mafunso okhudza ciphunzitso ca m’Baibo. Mafunso amenewo ali ku Zakumapeto “Gawo 1: Zimene Ife Akhristu Timakhulupilila.” Popeza kuti “Gawo 2: Umoyo Wacikhristu” ili na nkhani zofuna kusamala nazo, mkulu ndiye ayenela kusamalila mbaliyi.
11 Bungwe la akulu lingaone kuti pambuyo pa nthawi yakuti-yakuti, zingakhale zothandiza kumasinthako nchito za atumiki othandiza. Komabe, kulola abale kusamalila maudindo awo kwa nthawi yaitaliko kuli na ubwino wake. Amafika poidziŵa bwino nchitoyo na kuisamalila mwaluso.
12 Malinga na mikhalidwe, pali maudindo ena amene angapatsidwe kwa atumiki othandiza amene kupita kwawo patsogolo kwafika poonekela bwino kwa “anthu onse.” (1 Tim. 4:15) Ngati akulu ni ocepa pampingo, mtumiki wothandiza angaikidwe kukhala wothandizila woyang’anila kagulu, kapena kutumikila monga mtumiki wa kagulu, koma moyang’anilidwa na akulu. Atumiki othandiza angamapatsidweko mbali zina za Msonkhano wa Umoyo na Utumiki, kutsogoza Phunzilo la Baibo la Mpingo ngati pafunikila kutelo, komanso kukamba nkhani za anthu onse. Palinso nchito zina zimene zingapatsidwe kwa atumiki othandiza ngati pakhala kusoŵa, komabe akhale oti akukwanilitsa ziyenelezo za nchitoyo. (1 Pet. 4:10) Pothandizila akulu, atumiki othandiza ayenela kumadzipeleka na mtima wonse.
13 Ngakhale kuti nchito za atumiki othandiza n’zosiyana na zija za akulu, nazonso ni utumiki wopatulika kwa Mulungu, ndipo zimathandiza kuti mpingo uziyenda bwino. Ngati atumiki othandiza apitiliza kusamalila bwino maudindo awo, m’kupita kwa nthawi amayenelela kutumikila monga abusa komanso aphunzitsi. Zikatelo, amayenelezedwa kukhala akulu.
14 Ngati ndimwe m’bale wacinyamata, kapena munabatizika caposacedwa, kodi mukukalamila kuti mukakhale mtumiki wothandiza? (1 Tim. 3:1) Caka ciliconse, anthu ambili-mbili amabwela m’coonadi. Conco, pakufunikila amuna ambili oyenelela kuuzimu kuti asamalile maudindo mumpingo. Mungakalamile mwa kukhala na cikhumbo cofuna kuthandiza ena. Njila imodzi yocitila zimenezi ni kusinkha-sinkha pa citsanzo cabwino ca Yesu. (Mat. 20:28; Yoh. 4:6, 7; 13:4, 5) Pamene mupeza cimwemwe cobwela mwa kupatsa, cikhumbo cimeneco cidzakulila-kulila. (Mac. 20:35) Conco, khalani wodzipeleka pa kuthandiza ena, kusamalila Nyumba ya Ufumu, kapena kumakonzekela kuti muzikambako nkhani zogwilizila m’sukulu pa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki. Kukalamila kumaphatikizaponso kukulitsa makhalidwe auzimu, mwa kukhala na phunzilo laumwini lokhazikika. (Sal. 1:1, 2; Agal. 5:22, 23) Cinanso, m’bale amene akukalamila udindo amakhala wodalilika, ndiponso wokhulupilika pa nchito zimene amapatsidwa mumpingo.—1 Akor. 4:2.
15 Atumiki othandiza amaikidwa na mzimu woyela kuti azigwila nchito zopindulitsa mpingo. Onse mumpingo angaonetse kuti amayamikila nchito za atumiki othandiza pogwilizana nawo pamene akugwila nchito zawo. Mwanjila imeneyi, mpingo umaonetsa kuyamikila makonzedwe a Yehova amenewa, othandiza kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo m’gulu lake.—Agal. 6:10.