LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 16
  • Kodi Atumiki Othandiza Ali ndi Udindo Wanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Atumiki Othandiza Ali ndi Udindo Wanji?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • Atumiki Othandiza Amacita Utumiki Wofunika
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Muzionetsa kuti Mumayamikila “Mphatso za Amuna”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Abale​—Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukayenelele Kukhala Mtumiki Wothandiza?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi Akulu Amatumikila Mpingo m’Njila Ziti?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 16

PHUNZILO 16

Kodi Atumiki Othandiza Ali ndi Udindo Wanji?

Mtumiki wothandiza agaŵila mabuku

Ku Myanmar

Mtumiki wothandiza akukamba nkhani

Akamba nkhani

Mtumiki wothandiza akucititsa msonkhano

Kagulu ka ulaliki

Mtumiki wothandiza akuyeletsa pa Nyumba ya Ufumu

Kuyeletsa pa Nyumba ya Ufumu

Baibo imafotokoza magulu aŵili a amuna acikristu amene ali ndi maudindo mumpingo—“oyang’anila ndi atumiki othandiza.” (Afilipi 1:1) Nthawi zambili, pamakhala abale angapo amene amatumikila pampingo uliwonse. Kodi atumiki othandiza amacita nchito yanji kaamba ka ubwino wathu?

Amathandiza bungwe la akulu. Atumiki othandiza ni amuna auzimu, ni odalilika, ndipo ni acangu pa nchito yao. Ena ni acinyamata, ndipo ena ni acikulile. Amagwila nchito zosiyana-siyana zokhudza kayendedwe ka gulu zimene zimafunika pampingo. Izi zimapatsa akulu mpata wosamalila maudindo ao ophunzitsa ndi kuŵeta.

Amagwila nchito zofunika. Atumiki othandiza ena amakhala akalinde amene nchito yao ni kulandila anthu onse obwela pamisonkhano. Ena amasamalila zolankhulila, amagaŵila mabuku, amasamalila maakaunti, ndipo ena amagaŵila abale ndi alongo mumpingo magao olalikila. Amathandizanso pa nchito yokonza Nyumba ya Ufumu. Akulu angapemphe atumiki othandiza kuti asamalile okalamba. Atumiki othandiza ni okonzeka kucita nchito iliyonse imene apatsidwa, ndipo mpingo umawalemekeza cifukwa ca khama lao ndi mtima wao wokonda kutumikila ena.—1 Timoteyo 3:13.

Amapeleka citsanzo cabwino monga amuna acikristu. Atumiki othandiza amasankhidwa cifukwa ca makhalidwe ao auzimu. Nkhani zao pamisonkhano zimalimbitsa cikhulupililo cathu. Iwo amatsogolela pa nchito yolalikila, ndipo citsanzo cao cimaonjezela cangu cathu. Cifukwa ca mzimu wao wogwilizanika, amalimbikitsa cimwemwe ndi umodzi pampingo. (Aefeso 4:16) M’kupita kwa nthawi, naonso angayenelele kukhala akulu.

  • Kodi atumiki othandiza ni amuna otani?

  • Kodi atumiki amacita nchito ziti kuti zinthu ziziyenda bwino pampingo?

DZIŴANI ZAMBILI

Mukapita ku Nyumba ya Ufumu, muziyesetsa kudziŵana bwino ndi mkulu mmodzi kapena mtumiki wothandiza mmodzi kufikila mutawadziŵa onse ndi mabanja ao.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani