September 2-8
AHEBERI 7-8
Nyimbo 16 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Wansembe Mpaka Muyaya Monga mwa Unsembe wa Melekizedeki”: (10 min.)
Aheb. 7:1, 2—Melekizedeki, Mfumu komanso Wansembe, anakumana na Abulahamu na kumudalitsa (it-2 366)
Aheb. 7:3—Melekizedeki “analibe mzele wa mibadwo ya makolo” komanso “iye ndi wansembe kwamuyaya” (it-2 367 ¶4)
Aheb. 7:17—Yesu ni “wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki” (it-2 366)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Aheb. 8:3—Kodi pali kusiyana kwanji pakati pa mphatso na nsembe zimene zinali kupelekedwa m’Cilamulo ca Mose? (w00 8/15 14 ¶11)
Aheb. 8:13—Kodi pangano la Cilamulo linaleka bwanji kugwila “nchito” m’nthawi ya Yeremiya? (it-1 523 ¶5)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Aheb. 7:1-17 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Kuseŵenzetsa Bwino Zitsanzo Zooneka, ndiyeno kambilanani phunzilo 9 m’bulosha ya Kuphunzitsa.
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) it-1 524 ¶3-5—Mutu: Kodi cipangano catsopano n’ciani? (th phunzilo 7)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zimene Gulu Likukwanilitsa: (15 min.) Tambitsani vidiyo ya Zimene Gulu Likukwanilitsa ya September. Limbikitsani onse kukaonako likulu lathu kapena nthambi ya m’dziko lawo ngati n’kotheka.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 82
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 83 na Pemphelo