UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalidwe Loyela na Ulemu Waukulu Zimakopa Mtima
Khalidwe labwino la akazi okwatiwa amene anakhala okhulupilila, kambili limakopa amuna awo kubwela m’coonadi. Komabe, kucita izi kungafune kupilila mavuto kwa zaka zambili. (1 Pet. 2:21-23; 3:1, 2) Ngati mukucitilidwa zinthu zopanda cilungamo, pitilizani kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino. (Aroma 12:21) Citsanzo canu cingakhale na zotulukapo zabwino, ndipo cingathandize mwamuna wanu kukhala na maganizo oyenela ponena za coonadi.
Yesani kuona zinthu mmene mnzanu wa m’cikwati amazionela. (Afil. 2:3, 4) Khalani acifundo, ndipo citani zonse zimene mungathe kuti muzikwanilitsa maudindo anu monga mkazi wake. Khalani mvetseli wabwino. (Yak. 1:19) Khalani woleza mtima, ndipo muzimuonetsa mnzanu wa m’cikwati kuti mumamukonda. Ngakhale kuti mnzanuyo sakucitilani zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu, dziŵani kuti Yehova amayamikila kukhulupilika kwanu.—1 Pet. 2:19, 20.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA AMATITHANDIZA PA MAVUTO, NDIYENO, YANKHANI MAFUNSO AYA:
Kodi zinthu zinali bwanji poyamba m’cikwati ca mlongo Grace Li?
N’ciani cinamukopa kuti ayambe kuphunzila coonadi?
Kodi Mlongo Li anapilila mavuto abwanji pambuyo pobatizika?
Kodi mlongo Li anam’pemphelela ciani mwamuna wake?
Ni madalitso anji amene Mlongo Li akusangalala nawo cifukwa cokhala na khalidwe loyela ndiponso ulemu waukulu?
Khalidwe loyela na ulemu waukulu n’zamphamvu kwambili!