CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 3-5
Zotulukapo Zoipa za Bodza Loyamba
3:1-6, 15-19
Satana wakhala akusoceletsa anthu kucokela pamene ananamiza Hava. (Chiv. 12:9) Kodi mabodza otsatilawa amene Satana amacilikiza atsekeleza bwanji anthu kuyandikila Yehova?
Kulibe Mulungu wamphamvuzonse
Mulungu ni Utatu Wosamvetsetseka
Mulungu alibe dzina
Mulungu amalanga anthu m’moto wa helo kwamuyaya
Zonse zimene zimacitika n’cifunilo ca Mulungu
Mulungu sasamala za anthu
Kodi mumamvela bwanji mukaganizila mabodza onyoza Mulungu amenewa?
Kodi mungathandizile bwanji pa kuyeletsa dzina la Mulungu?