January 13-19
GENESIS 3-5
Nyimbo 72 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Zotulukapo Zoipa za Bodza Loyamba”: (10 min.)
Gen. 3:1-5—Mdyelekezi ananeneza Mulungu (w17.02 5 ¶9)
Gen. 3:6—Adamu na Hava sanamvele Mulungu (w00 11/15 25-26)
Gen. 3:15-19—Mulungu anaweluza opandukawo (w12 9/1 4 ¶2; w04 1/1 29 ¶2; it-2 186)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 4:23, 24—N’cifukwa ciani Lameki anakonza ndakatulo iyi? (it-2 192 ¶5)
Gen. 4:26—Kodi mwacionekele anthu a m’nthawi ya Enosi anayamba “kuitanila pa dzina la Yehova” motani? (it-1 338 ¶2)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 4:17–5:8 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela mafunso aya: N’ciani cimene mwakondapo na mmene wofalitsa wakambila mawu oyamba? Tikaona mmene ofalitsa apangila makonzedwe a ulendo wobwelelako, tiphunzilapo ciani?
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 1)
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso, kopani cidwi cake. (th phunzilo 3)
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo, ndiyeno gaŵilani magazini ya posacedwa yogwilizana na nkhani imene mwakambilana na mwininyumba. (th phunzilo 2)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Mmene Tingayambitsile Makambilano Pogwilitsila Nchito Mathirakiti”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani na kukambilana vidiyo yoonetsa mmene tingayambitsile makambilano poseŵenzetsa kathirakiti.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 99
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 85 na Pemphelo